Ezekiel 33:30 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Koma kunena za iwe, mwana wa munthu, anthu a mtundu wako amalankhula za iwe, akamakumana pafupi ndi makoma a mzinda ndi pa makomo a nyumba zao. Amauzana kuti, ‘Tiyeni tsopano tikamve zimene Chauta wanena.’
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo iwe wobadwa ndi munthu, ana a anthu a mtundu wako anena za iwe kumakoma ndi kumakomo a nyumba zao, nanenana yense ndi mbale wake, ndi kuti, Tiyeni tikamve mau ofuma kwa Yehova.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Koma kunena za iwe, mwana wa munthu, anthu a mtundu wako akumayankhula za iwe akakhala pa makoma a mzinda ndi pa makomo a nyumba zawo. Akumawuzana kuti, ‘Tiyeni tikamve uthenga umene wachokera kwa Yehova.’
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo iwe wobadwa ndi munthu, ana a anthu a mtundu wako anena za iwe ku makoma ndi ku makomo a nyumba zao, nanenana yense ndi mbale wace, ndi kuti, Tiyeni tikamve mau ofuma kwa Yehova.