Ezekiel 33:31 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Anthu anga amadzasonkhana kwa iwe nakhala pansi kuti amve zimene iweyo unene. Koma akazimva, sazitsata zimenezo. Zokamba zao zimaonetsa chikondi, m'menemo mitima yao imangokonda phindu chabe.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo akudzera monga amadzera anthu, nakhala pansi pamaso pako ngati anthu anga, namva mau ako, koma osawachita; pakuti pakamwa pao anena mwachikondi, koma mtima wao utsata phindu lao.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Anthu anga amabwera kwa iwe, monga momwe amachitira nthawi zonse anthu anga, ndipo amakhala pansi pamaso pako kumvetsera mawu ako. Koma zimene akumvazo sazichita. Zokamba zawo zimaonetsa chikondi, koma mitima yawo imakhala pa phindu lawo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo akudzera monga amadzera anthu, nakhala pansi pamaso pako ngati anthu anga, namva mau ako, koma osawacita; pakuti pakamwa pao anena mwacikondi, koma mtima wao utsata phindu lao.