Ezekiel 33:32 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kwa iwowo sindiwe kanthu konse, ndiwe munthu wamba chabe womangoimba nyimbo zachikondi ndi liwu lokoma poimba zeze. Kumva amamva mau ako onse, koma saŵagwiritsa ntchito.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo taona, akuyesa iwe ngati nyimbo yachikondi ya woimba bwino, woimba limba bwino; pakuti akumva mau ako, koma osawachita.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kunena zoona, kwa iwowo sindiwe kanthu konse, ndiwe munthu wamba chabe womangoyimba nyimbo zachikondi ndi liwu lokoma poyimba zeze. Kumva amamva mawu ako koma sawagwiritsa ntchito.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo taona, akuyesa iwe ngati nyimbo yacikondi ya woyimba bwino, woyimba limba bwino; pakuti akumva mau ako, koma osawacita.