Ezekiel 33:6 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma mlonda akaona mdani akubwera, iye osaliza lipenga kuti achenjeze anthu, tsono mdani nkubwera napha munthu wina, ngakhale kuti munthuyo wafera machimo ake, Ine ndidzamzenga mlandu mlonda uja chifukwa cha imfa ya mnzakeyo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma mlonda akaona lupanga likudza, osaomba lipenga, osachenjeza anthu, nilidza lupanga, nilichotsa mwa iwo; munthu atengedwadi m'mphulupulu zake, koma mwazi wake ndidzaufunsa pa dzanja la mlonda.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma ngati mlondayo aona lupanga likubwera ndipo osawomba lipengalo kuchenjeza anthu, ndipo lupanga libwera ndi kuchotsa moyo wa mmodzi mwa iwo, munthu ameneyo adzafa chifukwa cha tchimo lake, koma ndidzamuyimba mlandu mlondayo chifukwa cha imfa ya mnzakeyo.’
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma mlonda akaona lupanga likudza, osaomba lipenga, osacenjeza anthu, nilidza lupanga, nilicotsa mwa iwo; munthu atengedwadi m'mphulupulu zace, koma mwazi wace ndidzaufunsa pa dzanja la mlonda.