Ezekiel 33:8 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndikauza munthu woipa kuti, ‘Munthu woipa iwe, udzafa,’ iwe nupanda kumchenjeza kuti aleke makhalidwe oipa, kuti akhalebe ndi moyo, munthuyo adzafadi ali wochimwa, koma iweyo ndidzakuzenga mlandu chifukwa cha imfa yake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndikati Ine kwa woipa, Woipawe, udzafa ndithu, osanena iwe kumchenjeza woipayo aleke njira yake, woipa uyo adzafa m'mphulupulu yake, koma mwazi wake ndidzaufunsa pa dzanja lako.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndikawuza munthu woyipa kuti, ‘Iwe munthu woyipa, udzafa ndithu,’ ndipo iwe osayankhula kumuchenjeza kuti aleke njira zake, munthu wochimwayo adzafa chifukwa cha tchimo lake, koma Ine ndidzakuyimba mlandu chifukwa cha imfa yake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndikati Ine kwa woipa, Woipawe, udzafa ndithu, osanena iwe kumcenjeza woipayo aleke njira yace, woipa uyo adzafa m'mphulupulu yace, koma mwazi wace ndidzaufunsa pa dzanja lako.