Ezekiel 34:10 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndikuti, Ndaipidwa nanu abusanu. Ndidzakulandani nkhosa zanga, simudzazidyetsanso. Ndidzakuchotsani pa ntchito yaubusa, kuti musadzasamalenso za inu nokha. Ndidzapulumutsa nkhosa zanga kukamwa kwanu, ndipo simudzazidyanso.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Atero Ambuye Yehova, Taonani, Ine ndiipidwa nao abusa, ndidzafunsa nkhosa zanga pa dzanja lao, ndi kuwaletsa asadyetsenso nkhosazo, ngakhale kudzidyetsa okha sadzachitanso; ndipo ndidzalanditsa nkhosa zanga pakamwa pao, zisakhale chakudya chao.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ine Ambuye Yehova ndikuti: Ine ndayipidwa nanu, inu abusa. Ndidzakulandani nkhosa zanga ndipo simudzazidyetsanso. Ndidzakuchotsani pa ntchito ya ubusa kuti musamangodzidyetsa nokha. Ndidzalanditsa nkhosa zanga kukamwa kwanu ndipo simudzazidyanso.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Atero Ambuye Yehova, Taonani, Ine ndiipidwa nao abusa, ndidzafunsa nkhosa zanga pa dzanja lao, ndi kuwaletsa asadyetsenso nkhosazo, ngakhale kudzidyetsa okha sadzacitanso; ndipo ndidzalanditsa nkhosa zanga pakamwa pao, zisakhale cakudya cao.