Ezekiel 34:12 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Monga mbusa amanka nafunafuna nkhosa zake, pamene zina zabalalikira kutali, Inenso ndidzatero, kunka ndikufunafuna nkhosa zanga. Ndidzazipulumutsa konse kumene zidamwazikira pa nthaŵi yamdima ndi yankhungu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Monga mbusa afunafuna nkhosa zake tsiku lokhala iye pakati pa nkhosa zake zobalalika, momwemo ndidzafunafuna nkhosa zanga; ndipo ndidzawalanditsa m'malo monse anabalalikamo tsiku la mitambo ndi la mdima.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Monga mʼbusa amanka nafunafuna nkhosa zake pamene zina zabalalikira kutali, moteronso Ine ndidzafunafuna nkhosa zanga. Ndidzazipulumutsa kuchoka kumalo onse kumene zinabalalikira pa nthawi yankhungu ndi mdima.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Monga mbusa afunafuna nkhosa zace tsiku lokhala iye pakati pa nkhosa zace zobalalika, mamwemo ndidzafunafuna nkhosa zanga; ndipo ndidzawalanditsa m'malo monse anabalalikamo tsiku la mitambo ndi la mdima.