Ezekiel 34:13 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndidzazitulutsa pakati pa mitundu yonse ya anthu, ndidzazisonkhanitsa kuchokera ku maiko ena, ndipo ndidzazibwezera ku dziko lakwao. Ndidzaziŵetera ku mapiri a ku Israele, pafupi ndi mitsinje yake, ndi ku malo onse abwino kumene anthu amakhalako.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ndidzazitulutsa mwa mitundu ya anthu, ndi kuzisonkhanitsa m'maiko, ndi kulowa nazo m'dziko lao; ndipo ndidzazidyetsa pa mapiri a Israele, patimitsinje, ndi ponse pokhala anthu m'dziko.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndidzazitulutsa pakati pa mitundu ya anthu ndi kuzisonkhanitsa kuchokera ku mayiko ena, ndipo ndidzazibwezera ku dziko lawo. Ndidzaziwetera ku mapiri a Israeli, mʼmbali mwa mitsinje ndi kumalo kumene kumakhala anthu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ndidzaziturutsa mwa mitundu ya anthu, ndi kuzisonkhanitsa m'maiko, ndi kulowa nazo m'dziko lao; ndipo ndidzazidyetsa pa mapiri a Israyeli, patimitsinje, ndi ponse pokhala anthu m'dziko.