Ezekiel 34:16 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Zotayika ndidzazifunafuna, zosokera ndidzazibweza, zopweteka ndidzazimanga mabala ake. Zofooka ndidzazilimbikitsa, koma zonenepa ndi zamphamvu ndidzaziwononga. Ndidzaŵeta nkhosa zanga mwachilungamo.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndidzafuna yotayika, ndi kubweza yopirikitsidwa, ndi kulukira chika yothyoka mwendo, ndikulimbitsa yodwalayo; koma yonenepa ndi yolimba ndidzaziononga, ndidzazidyetsa ndi chiweruzo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndidzafunafuna zotayika ndi kubweza zosochera. Ndidzamanga mabala a zopweteka ndi kulimbikitsa zofowoka. Koma zonenepa ndi zamphamvu ndidzaziwononga. Ndidzaweta nkhosazo mwachilungamo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndidzafuna yotayika, ndi kubweza yopitikitsidwa, ndi kulukira chika yotyoka mwendo, ndi kulimbitsa yodwalayo; koma yanenepa ndi yolimba ndidzaziononga, ndidzazidyetsa ndi ciweruzo.