Ezekiel 34:18 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kodi inu simukhutira kudya pa busa labwino? Nanga mumaponderezeranji zimene simudya? Kodi simukhutira kumwa madzi abwino? Nanga madzi amene simumwa mumaŵadetsereranji ndi mapazi anu?
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Kodi chikucheperani, kuti mwadya podyetsa pabwino? Muyenera kodi kupondereza ndi mapazi anu podyera panu potsala? Muyenera kumwa madzi odikha, ndi kuvundulira otsalawo ndi mapazi anu?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kodi sikukukwanirani kudya msipu wabwino kuti muzichita kuponderezanso msipu umene simunadyewo? Kodi simukhutira ndi kumwa madzi abwino kuti muzinka mudetsanso madzi otsalawo ndi mapazi anu?
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Kodi cikuceperani, kuti mwadya podyetsa pabwino? muyenera kodi kupondereza ndi mapazi anu podyera panu potsala? muyenera kumwa madzi ndikha, ndi kubvundulira otsalawo ndi mapazi anu?