Ezekiel 34:2 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Iwe mwana wa munthu, ulengeze mau oimba mlandu abusa a Israele. Ulengeze, uŵauze kuti ‘Zimene akunena Ambuye Chauta ndi izi: Tsoka kwa inu abusa a ku Israele, amene mumangodzisamala inu nokha. Kodi suja abusa amayenera kusamala nkhosa?
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Wobadwa ndi munthu iwe, Nenera motsutsa abusa a Israele; nenera, nuti nao abusawo, Atero Ambuye Yehova, Tsoka abusa a Israele odzidyetsa okha; kodi abusa sayenera kudyetsa nkhosa?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Iwe mwana wa munthu, yankhula mawu oyimba mlandu abusa a Israeli. Lengeza ndipo uwawuze kuti Ine Ambuye Yehova ndikuti, ‘Tsoka kwa abusa a Israeli amene mumangodzisamala nokha! Kodi abusa sayenera kusamalira nkhosa?
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Wobadwa ndi munthu iwe, Nenera motsutsa abusa a Israyeli; nenera, nuti nao abusawo, Atero Ambuye Yehova, Tsoka abusa a Israyeli odzidyetsa okha; kodi abusa sayenera kudyetsa nkhosa?