Ezekiel 34:25 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Ndidzapangana nazo chipangano chamtendere. Zilombo zonse zolusa ndidzazichotsa m'dziko, kuti nkhosa zanga zizidzakhala mwamtendere, ngakhale m'chipululu kapena m'thengo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ndidzapangana nazo pangano la mtendere, ndi kuleketsa zilombo zoipa m'dzikomo; ndipo zidzakhala mosatekeseka m'chipululu, ndi kugona kunkhalango.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“ ‘Ndidzapangana nazo pangano la mtendere. Ndidzachotsa mʼdzikomo zirombo zolusa. Choncho nkhosa zanga zidzakhala mu mtendere mu chipululu ngakhalenso mʼthengo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ndidzapangana nazo pangano la mtendere, ndi kuleketsa zirombo zoipa m'dzikomo; ndipo zidzakhala mosatekeseka m'cipululu, ndi kugona kunkhalango.