Ezekiel 34:26 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndidzakhazika anthu anga kufupi ndi phiri langa, ndipo ndidzaŵagwetsera mvula pa nthaŵi yake, mvula yake ya madalitso.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti ndidzaika izi ndi milaga yozungulira chitunda changa, zikhale mdalitso; ndipo ndidzavumbitsa mivumbi m'nyengo yake, padzakhala mivumbi ya madalitso.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndidzakhazika anthu anga pafupi ndi phiri langa loyera ndipo ndidzawadalitsa. Ndidzawagwetsera mvula pa nthawi yake ndipo idzakhala mvula ya madalitso.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti ndidzaika izi ndi miraga yozungulira citunda canga; zikhale mdalitso; ndipo ndidzabvumbitsa mibvumbi m'nyengo yace, padzakhala mibvumbi ya madalitso.