Ezekiel 34:27 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mitengo ya m'minda idzabereka zipatso, ndipo minda idzakhala ndi zokolola zake, tsono anthu adzakhala mwamtendere m'dziko lao. Adzadziŵa kuti Ine ndine Chauta, pamene ndidzathyole magoli ao ndi kuŵapulumutsa kwa amene adaŵagwira ukapolo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndi mitengo ya kuthengo idzapereka zobala zao, ndi nthaka idzapereka zipatso zake, ndipo adzakhazikika m'dziko mwao; ndipo adzadziwa kuti Ine ndine Yehova, nditadula zomangira goli lao, ndi kuwalanditsa m'manja mwa iwo akuwatumikiritsa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mitengo ya mʼminda idzabereka zipatso zake, ndipo nthaka idzakhala ndi zokolola zake. Anthu adzakhala mwamtendere mʼdziko lawo. Iwo adzadziwa kuti Ine ndine Yehova, pamene ndidzathyola magoli awo ndi kuwapulumutsa kuchoka mʼmanja mwa amene anawagwira ukapolo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndi mitengo ya kuthengo idzapereka zobala zao, ndi nthaka idzapereka zipatso zace, ndipo adzakhazikika m'dziko mwao; ndipo adzadziwa kuti Ine ndine Yehova, nditadula zomangira goli lao, ndi kuwalanditsa m'manja mwa iwo akuwatumikiritsa.