Ezekiel 34:28 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Anthu a mitundu ina sadzaŵafunkhanso, ndipo zilombo zakuthengo sizidzaŵadya. Adzakhala mwamtendere popanda wina woŵaopsa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo sadzakhalanso chakudya cha amitundu, ndi chilombo cha kuthengo sichidzawadyanso; koma adzakhala osatekeseka, opanda wina wakuwaopsa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Anthu amitundu ina sadzawafunkhanso ndipo sadzadyedwa ndi zirombo zakuthengo. Adzakhala mwamtendere ndipo palibe amene adzawaopseze.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo sadzakhalanso cakudya ca amitundu, ndi cirombo ca kuthengo sicidzawadyanso; koma adzakhala osatekeseka, opanda wina wakuwaopsa.