Ezekiel 34:4 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nkhosa zofooka simudazilimbikitse, zodwala simudazichiritse, zopweteka simudazimange mabala ake, zosokera simudazibweze, ndipo zotayika simudazifunefune. Koma munkaziŵeta mozunza ndi mwankhalwe.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Zofooka simunazilimbitsa; yodwala simunaichiritsa, yothyoka simunailukira chika, yopirikitsidwa simunaibweza, yotayika simunaifuna; koma munazilamulira mwamphamvu ndi moopsa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Simunalimbitse nkhosa zofowoka, kapena kuchiritsa zodwala, kapena kumanga mabala a nkhosa zopweteka. Simunabweze zosochera kapena kufunafuna zotayika. Munaziweta mozunza ndi mwankhanza.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Zofoka simunazilimbitsa; yodwala simunaiciritsa, yotyoka simunailukira chika, yopitikitsidwa simunaibweza, yotayika simunaifuna; koma munazilamulira mwamphamvu ndi moopsa,