Ezekiel 34:8 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pali ine ndemwe, nkhosa zanga zidajiwa ndi zilombo zakuthengo, zidasanduka chakudya cha zilombo chifukwa chosoŵa abusa. Abusa anga sadalondole nkhosa zanga, ankangosamala za iwo okha, osasamala nkhosa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pali Ine, ati Ambuye Yehova, zedi, popeza nkhosa zanga zinakhala nyama, ndi nkhosa zanga zinakhala chakudya cha zilombo zonse za kuthengo, chifukwa kunalibe mbusa, ndi abusa anga sanafunafune nkhosa zanga, koma abusawo anadzidyetsa okha, osadyetsa nkhosa zanga;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pali Ine wamoyo, akutero Ambuye Wamphamvuzonse, ndithu, nkhosa zanga zinajiwa ndi zirombo zakuthengo, zinasanduka chakudya cha zirombo chifukwa panalibe abusa. Abusa anga sanafunefune nkhosa zanga. Iwo ankangosamala za iwo okha mʼmalo mosamala nkhosa zanga.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pali ine, ati Ambuye Yehova, zedi, popeza nkhosa zanga zinakhala nyama, ndi nkhosa zanga zinakhala cakudya ca zirombo zonse za kuthengo, cifukwa kunalibe mbusa, ndi abusa anga sanafunafuna nkhosa zanga, koma abusawo anadzidyetsa okha, osadyetsa nkhosa zanga;