Ezekiel 35:11 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono Ine Ambuye Mulungu ndikuti, Pali Ine ndemwe, ndidzakuchitani zomwe mudaŵachita anthu anga poŵaonetsa mkwiyo wanu, nsanje yanu ndi chidani chanu. Mudzandidziŵadi pakati panupo, ndikadzakulangani.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
chifukwa chake, Pali Ine, ati Ambuye Yehova, ndidzachita monga mwa mkwiyo wako, ndi monga mwa nsanje yako unachita nayo pa kukwiya nao iwe; ndipo ndidzadziwika nao pamene ndikuweruza.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Nʼchifukwa chake Ine Ambuye Yehova ndikuti: Pali Ine wamoyo, ndithu ndidzachita nanu monga munachita ndi anthu a ku Yuda ndi Israeli poonetsa mkwiyo wanu, nsanje yanu ndi chidani chanu pa iwo. Ndikadzakulangani mudzandidziwadi pakati panupo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
cifukwa cace, Pali Ine, ati Ambuye Yehova, ndidzacita monga mwa mkwiyo wako, ndi monga mwa nsanje yako unacita nayo pa kukwiya nao iwe; ndipo ndidzadziwika nao pamene ndikuweruza.