Ezekiel 35:15 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Monga momwe inu mudakondwera ndi kugwa kwa Israele, Ine ndidzakuchitaninso zomwezo. Iwe phiri la Seiri, ndi dziko lonse la Edomu, udzasanduka bwinja. Motero anthu onse adzadziŵa kuti Ine ndine Ambuye Mulungu.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Monga momwe unakondwerera cholowa cha nyumba ya Israele, popeza chidapasuka, momwemo ndidzakuchitira iwe; udzakhala wopasuka, phiri la Seiri iwe, ndi Edomu lonse lonseli; motero adzadziwa kuti Ine ndine Yehova.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Monga momwe inu munasangalala pamene anthu anga Aisraeli anagwa, Inenso ndidzakuchitani chimodzimodzi. Udzasanduka bwinja, iwe Phiri la Seiri, iwe ndi dziko lonse la Edomu. Zikadzatero anthu onse adzadziwa kuti Ine ndine Yehova.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Monga momwe unakondwerera colowa ca nyumba ya Israyeli, papeza cidapasuka, momwemo ndidzakucitira iwe; udzakhala wopasuka, phiri la Seiri iwe, ndi Edomu lonse lonseli; motero adzadziwa kuti Ine ndine Yehova.