Ezekiel 35:3 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Anthu akumeneko uŵauze kuti zimene ndikunena Ine Ambuye Chauta ndi izi: “Inu anthu a ku mapiri a ku Seiri ndikudana nanu. Ndidzakumenyani ndi dzanja langa, ndidzasandutsa dziko lanu tsala ndi chipululu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
nuti nalo, Atero Ambuye Yehova, Taona, ndiipidwa nawe phiri la Seiri, ndipo ndidzakutambasulira dzanja langa, ndi kukusanduliza lachipululu ndi lodabwitsa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
awawuze anthu a kumeneko kuti zimene ndikuyankhula Ine Ambuye Yehova ndi izi: Inu anthu a ku mapiri a Seiri ndikudana nanu. Ndidzatambasula dzanja langa kulimbana nanu, ndipo ndidzasandutsa dziko lanu kukhala chipululu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
nuti nalo, Atero Ambuye Yehova, Taona, ndiipidwa nawe phiri la Seiri, ndipo ndidzakutambasulira dzanja langa, ndi kukusanduliza lacipululu ndi lodabwitsa.