Ezekiel 36:10 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndidzachulukitsa anthu mwa inu ndiponso m'dziko lonse la Israele. M'mizinda mudzakhalanso anthu, ndipo nyumba zonse zimene zidaali mabwinja zidzamangidwanso.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndipo ndidzakuchulukitsani anthu nyumba yonse ya Israele, yonseyi, ndi m'midzimo mudzakhala anthu, ndi kumabwinja kudzamangidwa midzi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndidzachulukitsa chiwerengero cha anthu anu, nyumba yonse ya Israeli. Mʼmizinda mudzakhalanso anthu ndipo mabwinja adzamangidwanso.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndipo ndidzakucurukitsirani anthu nyumba yonse ya Israyeli, yonseyi, ndi m'midzimo mudzakhala anthu, ndi kumabwinja kudzamangidwa midzi.