Ezekiel 36:11 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndidzachulukitsa anthu anu pamodzi ndi nyama zomwe. Adzachuluka ndithu ndipo adzabereka ana ambiri. Anthu okhala mwa inu ndidzaŵachulukitsa monga momwe adaliri kale, ndipo ndidzakuchitirani zabwino kuposa kale. Motero mudzadziŵa kuti Ine ndine Chauta.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ndidzakuchulukitsirani anthu ndi nyama; ndipo adzachuluka, nadzabalana; ndipo ndidzakhalitsa anthu pa inu, monga umo anakhalira kale, ndipo ndidzachitira inu zabwino koposa poyamba paja; motero mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndidzachulukitsa chiwerengero cha amuna pamodzi ndi ziweto zomwe, ndipo adzachuluka kwambiri ndi kubereka ana ambiri. Ndidzakhazika anthu mʼdzikomo monga analili kale, ndi kukulemeretsani kuposa kale. Pamenepo inu mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ndidzakucurukitsirani anthu ndi nyama; ndipo adzacuruka, nadzabalana; ndipo ndidzakhalitsa anthu pa inu, monga umo anakhalira kale, ndipo ndidzacitira inu zabwino koposa poyamba paja; motero mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova.