Ezekiel 36:12 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndidzalola kuti anthu ayende pa inu, ndiye kuti inuyo anthu anga Aisraele. Iwowo adzakhazikika pa inu, ndipo inuyo mudzakhala chuma chao. Simudzalandanso ana a mtundu wao.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ndidzayendetsa anthu pa inu, ndiwo anthu anga Israele; adzakhala nawe dziko laolao, ndipo udzakhala cholowa chao osafetsanso ana ao.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndidzachititsa anthu kuyenda pa inu, ndiye kuti inu anthu anga Aisraeli. Iwowo adzakhazikika pa inu, ndipo inu mudzakhala cholowa chawo. Simudzalandanso ana awo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ndidzayendetsa anthu pa inu, ndiwo anthu anga Israyeli; adzakhala nawe dziko lao lao, ndipo udzakhala colowa cao osafetsanso ana ao.