Ezekiel 36:17 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Munthu iwe, pamene Aisraele ankakhala m'dziko lao, adaliipitsa ndi makhalidwe oipa ndiponso ndi zochita zao. Ndidaona kuti makhalidwe ao anali onyansa pa za chipembedzo, ngati mkazi amene ali kunthaŵi yake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Wobadwa ndi munthu iwe, muja a nyumba ya Israele anakhala m'dziko mwao, analidetsa ndi njira yao, ndi machitidwe ao; njira yao pamaso panga inanga chidetso cha mkazi wooloka.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Iwe mwana wa munthu, pamene anthu a Israeli ankakhala mʼdziko lawolawo, analiyipitsa ndi makhalidwe awo ndiponso zochita zawo. Machitidwe awo pamaso panga anali onyansa pa zachipembedzo ngati msambo wa mkazi amene ali pa nthawi yake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Wobadwa ndi munthu iwe, muja a nyumba ya Israyeli anakhala m'dziko mwao, analidetsa ndi njira yao, ndi macitidwe ao; njira yao pamaso panga inanga cidetso ca mkazi wooloka.