Ezekiel 36:19 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndidaŵamwaza pakati pa anthu a mitundu ina, ndipo ndidaŵabalalitsira ku maiko osiyanasiyana. Ndidaŵalanga potsata makhalidwe ao ndi ntchito zao.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndipo ndinawabalalitsa mwa amitundu, namwazika m'maiko monga mwa njira yao; ndi monga mwa machitidwe ao ndinawaweruza.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndinawamwaza pakati pa anthu a mitundu ina ndipo anabalalikira mʼmayiko onse. Ndinawalanga molingana ndi makhalidwe awo ndi zochita zawo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndipo ndinawabalalitsa mwa amitundu, namwazika m'maiko monga mwa njira yao; ndi monga mwa macitidwe ao ndinawaweruza.