Ezekiel 36:20 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Atafika pakati pa anthu a mitundu inayo, kulikonse kumene ankapita, adaipitsa dzina langa loyera. Zidatero chifukwa anthu ponena za iwowo ankati, ‘Aŵa ndi anthu a Chauta, koma onani adachotsedwa ku dziko lake.’
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo pofika iwo kwa amitundu kumene anamukako, anadetsa dzina langa loyera; popeza anthu ananena za iwowa, Awa ndi anthu a Yehova, natuluka m'dziko mwake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Atafika kwa anthu a mitundu ina, kulikonse kumene anapitako, anayipitsa dzina langa loyera. Zinatero popeza anthu ponena za iwo ankanena kuti, ‘Awa ndi anthu a Yehova, komatu anachotsedwa ku dziko lake.’
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo pofika iwo kwa amitundu kumene anamukako, anadetsa dzina langa loyera; popeza anthu ananena za iwowa, Awa ndi anthu a Yehova, naturuka m'dziko mwace.