Ezekiel 36:21 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Komabe Ineyo ndinkadera nkhaŵa dzina langa loyera, limene Aisraele adaliipitsa pamene ankakhala pakati pa anthu a mitundu ina kumene adapita.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma ndinawaleka chifukwa cha dzina langa loyera, limene a nyumba ya Israele adalidetsa pakati pa amitundu, kumene adamkako.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma Ine ndinkadera nkhawa dzina langa loyera, limene Aisraeli analiyipitsa pakati pa anthu a mitundu ina kumene anapitako.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma ndinawaleka cifukwa ca dzina langa loyera, limene a nyumba ya Israyeli adalidetsa pakati pa amitundu, kumene adarakako,