Ezekiel 36:22 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Nchifukwa chake Aisraelewo uŵauze kuti Ine Ambuye Chauta mau anga ndi aŵa: Zimene nditi ndichite, sindichita chifukwa cha inuyo Aisraelenu ai, koma chifukwa cha dzina langa loyera limene mudaliipitsa pakati pa anthu a mitundu ina kumene mudapita.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chifukwa chake nena kwa nyumba ya Israele, Atero Ambuye Yehova, Sindichichita ichi chifukwa cha inu, nyumba ya Israele, koma chifukwa cha dzina langa loyera munaliipsalo pakati pa amitundu, kumene mudamukako.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Nʼchifukwa chake awuze Aisraeliwo kuti Ine Ambuye Yehova ndikuti: Ine ndidzachita zimene ndidzachitezo osati chifukwa cha inuyo Aisraelinu ayi, koma chifukwa cha dzina langa, limene mwaliyipitsa pakati pa anthu a mitundu ina kumene munapitako.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Cifukwa cace nena kwa nyumba ya Israyeli, Atero Ambuye Yehova, Sindicicita ici cifukwa ca inu, nyumba ya Israyeli, koma cifukwa ca dzina langa loyera munaliipsalo pakati pa amitundu, kumene mudamukako.