Ezekiel 36:23 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Dzina langa lotchuka limene lakhala lonyozeka pakati pa anthu a mitundu ina, ndidzaonetsa kuti nloyera. Tsono anthu a mitundu inayo atazindikira kuti ndaonetsa kuyera kwa dzina langa mwa inu, adzadziŵa kuti Ine ndine Chauta. Ndikutero Ine Ambuye Chauta.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ndidzazindikiritsa dzina langa lalikulu kuti lili loyera, limene laipitsidwa mwa amitundu, limene inu munaliipsa pakati pao; ndipo amitundu adzadziwa kuti Ine ndine Yehova, ati Ambuye Yehova, pozindikiridwa Ine woyera mwa inu pamaso pao.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndidzaonetsa chiyero cha dzina langa lotchuka, limene layipitsidwa pakati pawo. Anthu a mitundu inayo atadzazindikira kuti ndaonetsa kudzera mwa inu kuti dzina langa ndi loyera, iwo adzadziwanso kuti Ine ndine Yehova. Ndikutero Ine Ambuye Yehova.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ndidzazindikiritsa dzina langa lalikuru kuti liri loyera, limene laipitsidwa mwa amitundu, limene inu munaliipsa pakati pao; ndipo amitundu adzadziwa kuti Ine ndine Yehova, ati Ambuye Yehova, pozindikiridwa Ine woyera mwa inu pamaso pao.