Ezekiel 36:26 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndidzakupatsani mtima watsopano ndi kuloŵetsa mzimu watsopano mwa inu. Ndidzakuchotserani mtima wanu wouma ngati mwalawo ndi kukupatsani mtima wofeŵa ngati mnofu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ndidzakupatsani mtima watsopano, ndi kulonga m'kati mwanu mzimu watsopano; ndipo ndidzachotsa mtima wamwala m'thupi, ndi kukupatsani mtima wamnofu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndidzakupatsani mtima watsopano ndi kulowetsa mzimu watsopano mwa inu. Ndidzachotsa mwa inu mtima wanu wowuma ngati mwala ndi kukupatsani mtima wofewa ngati mnofu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ndidzakupatsani mtima watsopano, ndi kulonga m'kati mwanu mzimu watsopano; ndipo ndidzacotsa mtima wamwala m'thupi, ndi kukupatsani mtima wamnofu.