Ezekiel 36:3 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndiye tsono iwe ulengeze ndi kuŵauza kuti ‘Zimene ndikunena Ine Ambuye Chauta ndi izi: Pamene adani anu adakusandutsani chipululu ndi kukuponderezani ku mbali zonse, mpaka inu kukhala m'manja mwa anthu a mitundu ina yonse, anthu ankakunenani ndi kukujedani.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
chifukwa chake unenere, nuti, Atero Ambuye Yehova, Chifukwa, inde chifukwa kuti anakupasulani, nakumemezani pozungulira ponse, kuti mukhale cholowa cha amitundu otsala, ndipo mwafika pa milomo ya akazitape, ndi pa mbiri yoipa ya anthu;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Choncho nenera ndipo uwawuze kuti, ‘Ine Ambuye Yehova ndikuti: Popeza anakusakazani ndi kukuponderezani ku mbali zonse motero kuti munakhala mʼmanja mwa anthu a mitundu ina yonse ndipo anthu ankakunenani ndi kukunyozani,
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
cifukwa cace unenere, nuti, Atero Ambuye Yehova, Cifukwa, inde cifukwa kuti anakupasulani, nakumemezani pozungulira ponse, kuti mukhale colowa ca amitundu otsala, ndipo mwafika pa milomo ya akazitape, ndi pa mbiri yoipa ya anthu;