Ezekiel 36:30 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndidzabereketsa mitengo zipatso zambiri ndipo nthaka idzabala zokolola zambiri, kotero kuti simudzanyozekanso chifukwa cha njala pakati pa anthu a mitundu ina.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ndidzachulukitsa zobala za mitengo, ndi zipatso za m'munda, kuti musalandirenso chitonzo cha njala mwa amitundu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndidzachulukitsa zipatso za mʼmitengo yanu ndi zokolola za mʼmunda mwanu, kotero kuti simudzanyozedwanso pakati pa anthu a mitundu ina chifukwa cha njala.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ndidzacurukitsa zobala za mitengo, ndi zipatso za m'munda, kuti musalandirenso citonzo ca njala mwa amitundu.