Ezekiel 36:31 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Apo mudzakumbukira makhalidwe anu oipa ndi ntchito zanu zoipa. Mudzachita manyazi chifukwa cha machimo anu ndi zonyansa zimene mudachita.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamenepo mudzakumbukira njira zanu zoipa, ndi zochita inu zimene sizinali zabwino; ndipo mudzanyansidwa nokha pamaso panu, chifukwa cha mphulupulu zanu ndi zonyansa zanu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pamenepo mudzakumbukira makhalidwe anu oyipa ndi ntchito zanu zoyipa. Machimo anu ndi ntchito zanu zonyansa zidzakuchititsa nokha manyazi.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamenepo mudzakumbukila njira zanu zoipa, ndi zocita inu zimene sizinali zabwino; ndipo mudzanyansidwa nokha pamaso panu, cifukwa ca mphulupulu zanu ndi zonyansa zanu.