Ezekiel 36:32 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndiyetu dziŵani kuti sindidzachita zimenezi chifukwa cha inuyo ai. Ndikutero Ine Ambuye Chauta. Choncho Aisraele inu, chitani manyazi, ndipo mugwetse nkhope chifukwa cha makhalidwe anu oipa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Dziwani kuti sindichita ichi chifukwa cha inu, ati Ambuye Yehova; chitani manyazi, dodomani, chifukwa cha njira zanu, nyumba ya Israele inu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsono dziwani kuti Ine sindidzachita zimenezi chifukwa cha inuyo ayi, ndikutero Ine Ambuye Wamphamvuzonse. Ndiyetu chitani manyazi ndipo mugwetse nkhope zanu, inu Aisraeli chifukwa cha makhalidwe anu!
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Dziwani kuti sindicita ici cifukwa ca inu, ati Ambuye Yehova; citani manyazi, dodomani, cifukwa ca njira zanu, nyumba ya Israyeli inu.