Ezekiel 36:35 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Motero anthu azidzati, ‘Dziko lija lidaali tsalali lasanduka ngati munda wa Edeni. Tsopano mukukhala anthu m'mizinda imene kale idaali mabwinja yosiyidwa ndi yoonongeka. Ndiponso mizindayo tsopano ili ndi malinga olimba.’
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo adzati, Dziko ili lachipululu lasanduka ngati munda wa Edeni ndi midzi yamabwinja, ndi yachipululu, ndi yopasuka, yamangidwa malinga, muli anthu m'mwemo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iwo adzati, ‘Dziko ili, limene linali chipululu, lasanduka munda wa Edeni. Mizinda imene inali mabwinja osiyidwa ndi owonongedwa, tsopano ndi yotetezedwa ndi yokhalamo anthu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo adzati, Dziko ili lacipululu lasanduka ngati munda wa Edene, ndi midzi yamabwinja, ndi yacipululu, ndi yopasuka, yamangidwa malinga, muli anthu m'mwemo.