Ezekiel 36:38 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Adzachuluka ngati nkhosa za ku Yerusalemu zimene ankazipereka kale ku nsembe pa nthaŵi ya chikondwerero. Motero mizinda yao yamabwinja ija idzadzazadi ndi magulu a anthu, ndipo iwowo adzadziŵa kuti Ine ndine Chauta.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ngati nkhosa za nsembe, ngati nkhosa za ku Yerusalemu pa zikondwerero zake zoikika, momwemo midzi yamabwinja idzadzala nao magulu a anthu; motero adzadziwa kuti Ine ndine Yehova.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Adzachulukadi ngati nkhosa zomwe ankapereka ngati nsembe ku Yerusalemu pa nthawi za chikondwerero. Choncho mizinda ya mabwinja idzadzaza ndi anthu. Zikadzatero adzadziwa kuti Ine ndine Yehova.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ngati nkhosa za nsembe, ngati nkhosa za ku Yerusalemu pa madyerero ace oikika, momwemo midzi yamabwinja idzadzala nao magulu a anthu; motero adzadziwa kuti Ine ndine Yehova.