Ezekiel 36:4 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nchifukwa chake inu, mapiri a ku Israele, imvani zimene Ine Ambuye Chauta ndikuuza mapiri ndi magomo, zigwembe ndi zigwa, mabwinja ndi mizinda yosiyidwa imene akhala akuifunkha ndi kuinyoza anthu a mitundu yokuzungulirani.’ ”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
chifukwa chake, mapiri inu a Israele, imvani mau a Ambuye Yehova. Atero Ambuye Yehova kunena ndi mapiri, ndi zitunda, ndi mitsinje, ndi zigwa, ndi zipululu zopasuka, ndi midzi yamabwinja, imene yakhala chakudya ndi choseketsa amitundu otsala akuzungulira;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
choncho, inu mapiri a Israeli, imvani zimene Ine Ambuye Yehova ndikuwuza mapiri ndi magomo, zigwembe ndi zigwa, mabwinja ndi mizinda yosiyidwa imene yakhala ikufunkhidwa komanso kunyozedwa ndi anthu a mitundu ina okuzungulirani.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
cifukwa cace, mapiri inu a Israyeli, imvani mau a Ambuye Yehova. Atero Ambuye Yehova kunena ndi mapiri, ndi zitunda, ndi mitsinje, ndi zigwa, ndi zipululu zopasuka, ndi midzi yamabwinja, imene yakhala cakudya ndi coseketsa amitundu otsala akuzungulira;