Ezekiel 36:5 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Ine Ambuye Chauta ndikuti, Ndakhala ndikulankhula ndili ndi mkwiyo woopsa, kuŵaimba mlandu anthu a mitundu ina yonse, makamaka a ku Edomu. Iwoŵa, mwa chimwemwe chodzaza tsaya ndiponso monyoza, adalanda dziko langa kulisandutsa lao, ndi kutengeratu mabusa ake.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
chifukwa chake atero Ambuye Yehova, Zoonadi pa nsanje yanga yodya nayo moto ndinanena motsutsana nao amitundu otsala, ndi Edomu lonse, amene anadzipatsira dziko langa likhale cholowa chao ndi chimwemwe cha mtima wonse, ndi mtima wopeputsa, kuti alande zake zonse zikhale zofunkha.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsono Ine Ambuye Yehova ndikuti: Mu mkwiyo wanga woopsa ndinayankhula kuyimba mlandu mitundu ina yonse ya anthu makamaka a ku Edomu. Iwowa mwa chimwemwe chodzaza tsaya ndi mwa nkhwidzi analanda dziko langa ndi kulisandutsa lawo ndi kutengeratu dziko la msipu kukhala lawo.’
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
cifukwa cace atero Ambuye Yehova, Zoonadi pa nsanje yanga yodya nayo moto ndinanena motsutsana nao amitundu otsala, ndi Edomu lonse, amene anadzipatsira dziko langa likhale colowa cao ndi cimwemwe ca mtima wonse, ndi, mtima wopeputsa, kuti alande zace zonse zikhale zofunkha.