Ezekiel 36:6 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Nchifukwa chake ulengeze za dziko la Israele, ndipo uuze mapiri ndi magomo, zigwembe ndi zigwa, mau a Ine Ambuye Chauta, akuti, Ndikulankhula ndi mtima wokwiya kwambiri, chifukwa chakuti mudapirira manyozo ochokera kwa mitundu ina ya anthu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chifukwa chake unenere za dziko la Israele, nuti kwa mapiri ndi kwa zitunda, kwa mitsinje ndi kwa zigwa, Atero Ambuye Yehova, Taonani, ndalankhula mu nsanje yanga ndi ukali wanga, popeza mwasenza manyazi a amitundu;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Nʼchifukwa chake, lengeza ku dziko la Israeli, ndipo uwuze mapiri ndi magomo, zigwembe ndi zigwa kuti, ‘Ine Ambuye Yehova ndikuti: Ine ndikuyankhula ndi mtima wokwiya kwambiri chifukwa inu munalandira chitonzo cha anthu a mitundu ina.’
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Cifukwa cace unenere za dziko la Israyeli, nuti kwa mapiri ndi kwa zitunda, kwa mitsinje ndi kwa zigwa, Atero Ambuye Yehova, Taonani, ndalankhula mu nsanje yanga ndi ukali wanga, popeza mwasenza manyazi a amitundu;