Ezekiel 37:1 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mphamvu ya Chauta idandigwira, Mzimu wa Chauta udandinyamula nkukandikhazika pakati pa chigwa. Chigwacho chinali chodzaza ndi mafupa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Dzanja la Yehova linandikhalira, ndipo anatuluka nane mu mzimu wa Yehova, nandiika m'kati mwa chigwa, ndicho chodzala ndi mafupa;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Dzanja la Yehova linali pa ine, ndipo Mzimu wa Yehova unandinyamula nʼkukandikhazika pakati pa chigwa. Chigwacho chinali chodzaza ndi mafupa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Dzanja la Yehova linandikhalira, ndipo anaturuka nane mu mzimu wa Yehova, nandiika m'kati mwa cigwa, ndico codzala ndi mafupa;