Ezekiel 37:10 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Motero ndidayamba kulalika monga adandilamulira. Tsono mpweya udaloŵa mwa iwo, ndipo akufa aja adakhala ndi moyo, naimirira. Linali gulu lalikulu kwambiri la ankhondo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
M'mwemo ndinanenera monga anandiuza, ndi mpweya unawalowa, ndipo anakhala ndi moyo, naimirira chilili, gulu la nkhondo lalikulukulu ndithu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Choncho ndinanenera monga anandilamulira ndipo mpweya unalowa mwa iwo; apo anthu akufawo anakhala ndi moyo, nayimirira ndipo linali gulu lalikulu lankhondo.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
M'mwemo ndinanenera monga anandiuza, ndi mpweya unawalowa, ndipo anakhala ndi moyo, naimirira ciriri, gulu la nkhondo lalikurukuru ndithu.