Ezekiel 37:16 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Iwe mwana wa munthu, tenga ndodo, ulembepo kuti, ‘Ya Ayuda ndi Aisraele ogwirizana nawo.’ Tsono utenge ndodo ina, ulembepo kuti, ‘Ya Aefuremu, ndiye kuti fuko la Yosefe, ndi Aisraele ogwirizana nawo.’
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Tsono, iwe wobadwa ndi munthu, Tenga mtengo umodzi, nulembepo, Wa Yuda ndi wa ana a Israele anzake; nutenge mtengo wina, nulembepo, Wa Yosefe, mtengo wa Efuremu, ndi wa nyumba yonse ya Israele anzake;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Iwe mwana wa munthu, tenga ndodo ndipo ulembepo kuti, ‘Ndodo ya Yuda ndi Aisraeli oyanjana nawo.’ Utengenso ndodo ina ndipo ulembepo kuti, ‘Ndodo ya Efereimu, ndiye kuti fuko la Yosefe ndi Aisraeli onse oyanjana nawo.’
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Tsono, iwe wobadwa ndi munthu, Tenga mtengo umodzi, nulembepo, Wa Yuda ndi wa ana a Israyeli anzace; nutenge mtengo wina, nulembepo, Wa Yosefe, mtengo wa Efraimu, ndi wa nyumba yonse ya Israyeli anzace;