Ezekiel 37:19 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
uŵauze kuti Ine Ambuye Chauta ndikuti, Ndili pafupi kutenga ndodo ya Yosefe, imene ili m'manja mwa Efuremu, pamodzi ndi Aisraele ogwirizana nawo, ndiilumikiza ndi ndodo ya Yuda kuti zikhale ndodo imodzi. Ndipo zidzakhaladi imodzi m'manja mwanga.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Unene nao, Atero Ambuye Yehova, Taonani, ndidzatenga mtengo wa Yosefe uli m'dzanja la Efuremu, ndi wa mafuko a Israele anzake, ndi kuwaika pamodzi ndi mtengo wa Yuda, ndi kuiyesa mtengo umodzi; ndipo idzakhala umodzi m'dzanja langa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
iwe udzawawuze mawu awa a Ine Ambuye Yehova akuti, ‘Ine ndidzatenga ndodo ya Yosefe imene ili mʼdzanja la Efereimu, ndi ya mafuko a Aisraeli oyanjana naye, ndi kuyilumikiza ku ndodo ya Yuda, kuti zikhale ndodo imodzi, ndipo zidzakhaladi ndodo imodzi mʼdzanja langa!’
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
unene nao, Atero Ambuye Yehova, Taonani, ndidzatenga mtengo wa Yosefe uli m'dzanja la Efraimu, ndi wa mafuko a Israyeli anzace, ndi kuwaika pamodzi ndi mtengo wa Yuda, ndi kuiyesa mtengo umodzi; ndipo idzakhala umodzi m'dzanja langa.