Ezekiel 37:21 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
pamenepo udzaŵauze kuti Ine Ambuye Chauta ndikuti, Ndidzaŵaitana Aisraele kuchokera ku malo ao aukapolo pakati pa anthu a mitundu ina. Ndidzaŵasonkhanitsa kuchokera ku mphepo zinai ndi kuŵabwezera ku dziko lao.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Nunene nao, Atero Ambuye Yehova, Taonani, ndidzatenga ana a Israele pakati pa amitundu kumene adamkako, ndi kuwasokolotsa kumbali zonse, ndi kulowa nao m'dziko mwao;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
udzawawuze kuti Ine Ambuye Yehova ndikuti: Ndidzawachotsa Aisraeli pakati pa anthu a mitundu ina kumene anapita ku ukapolo. Ndidzawasonkhanitsa kuchokera ku mbali zonse ndi kubwera nawo ku dziko lawolawo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Nunene nao, Atero Ambuye Yehova, Taonani, ndidzatenga ana a Israyeli pakati pa amitundu kumene adamkako, ndi kuwasokolotsa ku mbali zonse, ndi kulowa nao m'dziko mwao;