Ezekiel 37:22 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndidzaŵasandutsa mtundu umodzi m'dzikomo, ku mapiri a Israele, ndipo adzakhala ndi mfumu imodzi yokha. Sadzakhalanso mitundu iŵiri ya anthu kapena kugaŵikana maufumu aŵiri.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndipo ndidzawayesa mtundu umodzi m'dzikomo, pa mapiri a Israele; ndipo mfumu imodzi idzakhala mfumu ya iwo onse, sadzakhalanso mitundu iwiri, kapena kugawanikanso maufumu awiri konse ai.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndidzawasandutsa mtundu umodzi mʼdzikomo, pa mapiri a Israeli. Padzakhala mfumu imodzi yowalamulira, ndipo sadzakhalanso mitundu iwiri kapena kugawikana maufumu awiri.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndipo ndidzawayesa mtundu umodzi m'dzikomo, pa mapiri a Israyeli; ndipo mfumu imodzi idzakhala mfumu ya iwo onse, sadzakhalanso mitundu iwiri, kapena kugawanikanso maufumu awiri konse ai.