Ezekiel 37:23 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Sadzadziipitsanso ndi mafano ao ndi zinthu zina zonyansa, kapena ndi zochimwa zao zina zilizonse. Ndidzaŵapulumutsa ku machimo ao onse, ndipo ndidzaŵayeretsa. Motero iwowo adzakhala anthu anga, ndipo Ineyo ndidzakhala Mulungu wao.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo sadzadzidetsanso ndi mafano ao, kapena ndi zonyansa zao, kapena ndi zolakwa zao zilizonse; koma ndidzawapulumutsa mokhala mwao monse m'mene anachimwamo, ndi kuwayeretsa; m'mwemo adzakhala anthu anga, ndi Ine ndidzakhala Mulungu wao.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Sadzadziyipitsanso ndi mafano awo, kapena ndi zinthu zawo zonyansa, kapenanso ndi ntchito zawo zoyipa zilizonse. Ndidzawapulumutsa ku machimo awo onse ndi kuwayeretsa. Choncho adzakhala anthu anga, ndipo Ine ndidzakhala Mulungu wawo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo sadzadzidetsanso ndi mafano ao, kapena ndi zonyansa zao, kapena ndi zolakwa zao ziri zonse; koma ndidzawapulumutsa mokhala mwao monse m'mene anacimwamo, ndi kuwayeretsa; m'mwemo adzakhala anthu anga, ndi Ine ndidzakhala Mulungu wao.