Ezekiel 37:26 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndidzachita nawo chipangano chamtendere. Chipangano chimenechi chidzakhala chao mpaka muyaya. Ndidzaŵakhazikitsa ndi kuŵachulukitsa, ndipo ndidzaika Nyumba yanga pakati pao mpaka muyaya.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ndidzapangana nao pangano la mtendere, lidzakhala pangano losatha nao, ndipo ndidzawakhazika, ndi kuwachulukitsa, ndi kuika malo anga opatulika pakati pao kosatha.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndidzachita nawo pangano lamtendere; lidzakhala pangano lamuyaya. Ndidzawakhazikitsa ndi kuwachulukitsa, ndipo ndidzayika malo anga opatulika pakati pawo kwamuyaya.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ndidzapangana nao pangano la mtendere, lidzakhala pangano losatha nao, ndipo ndidzawakhazika, ndi kuwacurukitsa, ndi kuika malo anga opatulika pakati pao kosatha.