Ezekiel 37:7 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pamenepo ndidayamba kulalika monga momwe adandilamulira. Ndikulalika choncho ndidangomva kuti gogobedegogobede! Mafupa aja kuyamba kulumikizana.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
M'mwemo ndinanenera monga anandiuza, ndipo ponenera ine panali phokoso; ndipo taonani, panali gobedegobede, ndi mafupa anasendererana, fupa kutsata fupa linzake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo ndinanenera monga anandilamulira. Ndipo pamene ndinkanenera, ndinamva gobedegobede, ndipo mafupa aja anayamba kulumikizana, fupa ku fupa linzake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
M'mwemo ndinanenera monga anandiuza, ndipo ponenera ine panali phokoso; ndipo taonani, panali gobede gobede, ndi mafupa anasendererana, pfupa kutsata pfupa linzace.