Ezekiel 37:9 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono Chauta adandiwuza kuti, “Iwe mwana wa munthu, ulalike ndi kuuza mpweya mau a Ine Ambuye Chauta, akuti, ‘Mpweya iwe, bwera kuno, bwera kuchokera ku mphepo zinai, dzaŵauzire anthu ophedwaŵa, kuti akhalenso ndi moyo.’ ”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anati kwa ine, Nenera kwa mpweya, nenera, wobadwa ndi munthu iwe, nuti kwa mpweya, Atero Ambuye Yehova, Idza, mpweya iwe, kuchokera kumphepo zinai, nuuzire ophedwa awa, kuti akhale ndi moyo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsono Yehova anandiwuza kuti, “Nenera kwa mpweya, nenera iwe mwana wa munthu ndi kuwuza mpweya mawu a Ine Ambuye Yehova kuti, ‘Bwera kuno iwe mpweya. Bwera kuchokera ku mbali zonse zinayi ndi kudzawuzira anthu ophedwawa kuti akhalenso ndi moyo.’
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anati kwa ine, Nenera kwa mpweya, nenera, wobadwa ndi munthu iwe, nuti kwa mpweya, Atero Ambuye Yehova, Idza, mpweya iwe, kucokera ku mphepo zinai, nuuzire ophedwa awa, kuti akhale ndi moyo.