Ezekiel 38:11 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndipo udzanena kuti, ‘Ndikukathira nkhondo dziko la midzi yopanda malinga. Ndipita kwa anthu amene amakhala mwamtendere, amene satchinjirizidwa ndi malinga kapena zitseko kapena mipiringidzo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
nudzati, Ndidzakwera kunka kudziko la midzi yopanda malinga, ndidzamka kwa iwo amtendere okhala mosatekeseka, onsewo akukhala opanda malinga, opanda mapiringidzo, kapena zitseko;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iwe udzanena kuti, ‘Ndikukathira nkhondo dziko la midzi yopanda mipanda; ndikathira nkhondo anthu okhala mwamtendere, anthu amene satchinjirizidwa ndi mipanda, zipata kapena mipiringidzo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
nudzati, Ndidzakwera kumka ku dziko la midzi yopanda malinga, ndidzamka kwa iwo amtendere okhala mosatekeseka, onsewo akukhala opanda malinga, opanda mipingiridzo, kapena zitseko;